NGANGA YOPAMBANA ZONSE KUZAMBWE
International Writing Program ku Iowa inatilangiza dziko la America kupyolera mbali zosiyana-siyana. Monga tsiku lina, mu nyuzipepala ya University, kunalengezedwa kuti a Night Dancer Club, pamwamba pa asungwana khumi ndi mphambu zinai omwe amaonetsa chionetselo cha maliseche, kukhalanso wina dzina lake Candy Apples yemwe adzonetsa nganga yoposa zonse ku zambwe. Ngati timakhumbila kukaona ma philamidi kapena kuonana ndi Papa, choletsa chingakhale chiyani. Ndinayamuka kupita konko ndi anzanga.
Chipinda chachikulu cha Dancer Club chinakonzedwa motero kuti sizikanatheka kuphonyana ndi guleyo. Pakati-kati pachipindacho, panali malo omwe anakonzedwa kuti asungwana odzavina ndi kubvulawo adzifikile ndikuonetsa luso lawolo.
Candy Apples, katswiri wa usikuwo sanali wantali koma woumbidwa bwino. Monga katswiri, anali atabvala chovala chapamwamba choti chibvulidwe. Ngakhale anabvina kwa mphindi zochepa, anthu onse m’chipindachi anasangalala naye kwambiri. M.malo mongotola ndalama zomwe anali kusupidwa, ankatenga ndalamazo nkulowetsa m’mphuno ya amene wasupa uja kenaka mwa luso lapadera, amachotsa ndalama zija ndi mawere ake.
Sindikanachitira mwina koma kudzipeleka kuti mawere abwino chonchi, wopambana wonse ku zambwe atulutse ndalama m’mphuno zanga. Zinali zosangalatsa kwambiri ngati Mayi, akukakaniza thupi lache lofewa kumaso kwako. Ngakhale ndalama zimapita, zimapitila pa kaone.
Chonetserochi chitatha, Candy anayamba kugulitsa zithunzi zake. Sikuti ndinatengeka naye mtima, koma ndinkafuna nditadziwa zambiri za iye. Ndinayenera kuchitapo kanthu.
Ndinamudziwitsa zaine ndipo Candy anali wochezeka. Anayang’anitsitsa chitupa changa ndipo anakuwa: “Slovakia! Ndife abale. Dzina langa lene-leni ndi Halyna ndipo kwathu ndi ku Ukraine.”
Zoona anzanga. Nganga zabwino za ku zambwe zimachokera ku bvuma.
(Translated into Chichewa by Alfred Msadala)
1 comment:
Благодаря за интересната информация
Post a Comment